Adamu - Poem by Bonwell Rodgers

Ndilole ndimwe madzi a moyo pamilomo yako,
n'kudzuka ku tulo ta imfa ya mikwingwirima yanga.
Luso linapotedwa pamilomo yako,
chuma chinakolekedwa mtimaso tako tonga mkaka.
Ndiwe shuga woiwalitsa kuwawa.
Mchere wokometsera ndiwo.

Ndine wokonzeka kukupsopsona pamphambano pano,
kuti aliyense aone kuzama kwa chikondi changa.
Milomo yako igundane ndi yangayi,
ine n'kuledzera popanda vinyo, n'kuuluka popanda mapiko.
Milomo yako ikutentha bee, utaitseguka pang'ono
kwinaku utatsinzina n'kumaganizira ineyo.

Chonde bwera kuno getsi, duwa langa,
Ndipsospone ndidakali moyo,
Ndani akudziwa mawa kugwanji?
Usiku utalikirenji, mwina kulekana n'komweku.
N'kuloleranji kudzanong'oneza bondo mwayi ukuuona?
Nditatsamira mkono n'kulekana nazo zabwinozi.
Ndiyetu ndiukitsiretu ndi milomo yako.

Poems by Bonwell Rodgers

next poem »Transmuted Fowls
« prev poemMango

Add Comment